Home
     => Malawi weather-Zanyengo
     => Religion
     => Project Proposals
     => Nyimbo za kumalawi
     => Autobiography of Benie Mpaso junior
     => Zauzimu
     contacts
     Za chuma (Economy)
     Polls
     Total visitors
     Zamasewero-Sports
     Gallery
     music



SAY NO! TO NEPOTISM - Zauzimu


Kuchokera kale losne, mau akuti cholinga akhala akutanthauziridwa m‘njira zambiri. Matanthatuzidwe onsewa amachitika molingana ndi zomwe munthyuyo akufuna kukwaniritsa (kufikitsa pa zokhumba zamunthu) pa nthanwi imeneyo. Cholinga chenicheni cha mtundu wa anthu ndi kupitilizitsa zinthu zomwe zimaoneka ngati zikulamulira chilengedwe chozungulira malo omwe iye amapezeka. Pa zifukwa monga izi, anthu akhala akuyankhula zambiri zokhudza ntchito zosiyanasiyana. Mwa chitsanzo wina wake anati, "chinali cholinga changa kugula kapena kuchita zinthu za mtundu uwu". Komabe kuti munthu ameneyu timufunse kuti cholinga chake chobadwira iye ndi chiyani zotsatira zake iyeyu amakhala wopanda chonena.

 

Mu ndakaatulo iyi, ndikufuna kupeleka linagliro langa ndi kuyankha kwanga pa funso limeneli pofotokoza zinthu zingapo zokhudzana ndi nkhaniyi "Cholinga chamunthu ndi chiyani?"

Poyambilira penipeni nditanthauzira mau oti cholinga pogwilitsa ncthito nthathauzira mau otchedwa Chambers Dictionary; "Cholinga ndi zotsatira zoyembekezereka kuchokera kukugwira ntchito". Kutambasula mau amenewa mau anga ndinganene kuti cholinga ndi chiyambi chomwe chimalenga kapena kuti chomwe chimapangitsa zinthu kuti zikhale. Kuchokera mu kutanthauza kumeneku tikupeza kuti chifukwa cha cholinga, zinthu zonse zinapangidwa kuti zikhale m’mene ziliri. Nkukamba kwina tinangati chilichonse chomwe ife timaona pa dziko lino lapansi kaya kumlengalenga chipangidwa ndi cholinga.

 

Tiyenera kumvetsa bwino kuchokera kutanthauza kwa mau amenewa kuti Cholinga sichipezeka mu chopangidwa koma malingaliro awopangayo. Ena tayamba kale kudzifunsa kuti kodi izi nkutiphunzitsa ndithu? Taganizirani m’mene Baibulo limafotokozera; Kudzera mwa atumiki ake Yehova Mulungu wakhala akutiuza za cholinga chake cha kulenga. Ndipo limapitiliza kufotokoza kuti munthu anali m’modzi mwa zolinga za Yehova Mulungu mwini. Yehova anamukundikira munthu chiyang’aniro cha chilengedwe chonse monga bukhu la Genesis lifotokozera.

 

Tsopano , popeza cholinga cha chilengedwe chiri mwa Mulengi tiyenera kulingalira bwino podziwa kuti kuti munthu apezeke m’dziko lapansi chinali cholinga, ndipo cholinga chimenechi ndi chinali mwa mwini wake Yehova Mulungu. Izi zitathauza kuti Mulungu anali atakonzeratu zolenga Munthu asanamulenge munthuyo. Dziko la pansi ndi cholinga cha Mulungu chifukwa zinali malingaliro a Mulungu kuti munthu adzapeze pokhala. Chotero munthu akuyenera kukhala wosamalitsa pamene akulingalira zofuna kuchita m’dziko lino lapansi. Munthu sayenera kukonzerkera kuchita kanthu kopanda cholinga. Pa Aefeso1:3 tikumva kuti munthu ngodalitsidwa kwathunthu ndi madalisto a uzimu a mwambamwamba.

 

Dziko limadziwa kuti Yesu Khristu anakhalapo pa zdiko lino lapansi ndipo anafa kamba ka zochimwa za anthu am’dziko lapansi. Kodi Yesu anabwera liti padziko lino, Kufunsa funso la mtundu uwu kungaoneke ngati kutsutsana ndi zodziwikiratu chifukwa kudzera nkumasulira kwathu kwa mau oti cholinga tapeza ife nthawi yomwe Yesu anabwerera pa dziko lino lapansi. Mutanthauzo limeneli tapeza ife kuti Yesu anabadwa chifukwa anali atafa kale. Taganizirani m’mene muliri inu kuti ndinu thupi lopangiwa ndi tizidutswa tating’onoting’ono tomwe tinapangidwa moyandikana tomwe timamverana kena ndi kanzake. Izi zisonyezeratu kuti simunapezeke mwamwayi koma ndi cholinga cha Mulungu pa inu. (Eph1:11). Ngati kamodzi kqachita zinthu zosiyana ndi tinzake kamafa kapena tina totsatira tomwe tigundana nako timatsatira nato kakhalidwe kachilendoko ndipo iyi ndi nthenda yomwe imatchuka kuti Cancer lero lino.

Kuchokera pa zokambidwa pamwambapa tafokokozapo za dongosolo, kodi dongosolo ndi chain? Kuchokera pa lingaliro lomwe lija la cholinga, tingathe kutanthauziira ndondmeko ya dongosolo monga kutalika kwa pakatikati pa chiyambi ndi chimaliziro (Jer. 11) kuyambira vesi loyamba. Mulungu amagwira ntchito mu china chili chonse ndi cholinga chokwaniritsa zolinga zake. N’chifukwa chake timamva kuti Mulungu sanama( (Heb 6:18) ndiye popeza Mulungu sanama iye amatsata dongosolo la mfundo zake.

 

Machidule ndifotokozapo pang’ono ndondomeko zisanu ndi imodzi zomwe zingathe kumapngitsa munthu kizindikira Mulungu monga Yehova ndi Mulengi komanso zolinga za mulungu.

 

Chifukwa cha izi munthu anakhala:

1.IYE NDI MULUNGU WA CHOLINGA.(Gen 1:1)

2.CHILI CHONSE CHOLENGEDWA CHILI NDI CHOLINGA

 

3. SIZOLINGA ZONSE ZILI ZODZIWIKA KWA MUNTHU:

 

Munthu kwa zaka zambiri akhala akuononga chilengedwe pofuna kudziwa za cholinga chimene zinthu zimapezekera m’mene ziliri. Kamba kofuna kudiwa chifukwa chomwe zinthu zimapezeka m’maene zilirimu chilengedwe chambiri chapeza mavuto. Zolinga za mulungu sizifanana ndi zolinga zamunthu. Munthu mukupelewedwa kwake nzeru akhala akuononga chilengedwe ndicholinga choganiza kuti akufuna kuthetsa mavuto omwe iye akukumana nawo. Mwa chitsanzo munthawi zoyambilira zenizeni anthu sanazindikire cholinga chowe Mulungu anaikira dera la mphweya lolekanitsa lotchedwa Ozone kufikira anthu ataliononga dera lonselo nazindikira kufunika kwake. Ilipo nzeru yooneka ngati yopambana pamaso pa munthu ngati saikapo mulungu pa nzeruyo ndipo mapeto ake imtembenukira iye mwini.

 

4. NGATI CHOLINGA CHOSADZIWIKA KULAKWITSA KOYEMBEKEZEREKA.

Ichi ndi chifukwa chake anthu ambiri amapezeka kuti aononga miyoyo yawo. Lero lino anthu ambiri akukhala miyoyo wongoyerekeza chifukwa sadziwa cholinga cha miyoyo yawo ndi zifukwa zomwe zinthu zimapezekera. Mulungu sanalinge kuika miyala kuti idzakhale yopangira zida, mipeni ndi zida zina zoopsa. Mlengi mwini sanalenge zinthu ndi cholinga choti cha zidzakhale zoonongera zinzake kapena anthu.Koma kamba kosadziwa cholinga, kuchita zinthu molakwitsa kwachuluka padziko lapansi. Pa zifukwa izi padziko lapansi pali chipwilkikiti cha mapvuto. Pano ena ayamba kulimbana ndi anthu amene akumakumba miyala ya Uranium akadakhala kuti amadziwa cholinga chomwe adalengera Uranium, sibwenzi pali mavuto tikuwaona lero lino. Munthu angadziwe bwanji cholinga cha chinthu?

Tikaunguzaunguza (kuyang’anayang’ana mbali zonse) sitingathe kuona m’mene chilengewe chikugwiritsidwira ntchito molakwitsa kamba ka kusazindikira komwe kuli mwa ife. Ngati munthu afuna kudziwa cholinga cha chinthu njira yake ndi yofuna yoyamba wafuna wochipanga. Machitsanzo ngati mufuna kudziwa m’mene makina amtundu uli wonse amagwirira ntchito tiyenera kufunsa mwini wake wopangayo kuti atiuze m’mene agwiririra ntchito. Buku la Yohane 1:1 ikutilangiza ife kufunsa mwini chilengedwe.

5. NGATI SIMUKUDZIWA CHOLINGA CHAKE CHA CHINTHU MUSAYEREKEZE DALA KUCHITA KAPENA KUFUNSA CHINTHUCHO

 

Ndi chinthu choopsa kufunsa chinthu chopangidwa za m’mene chimagwilira ntchito kapena kuti chinapangidwiranji. Ndi kupusa kufunsa sopo chifukwa chomwe wapangidwira m’malko ofunsa kampnai yomwe yapanga sopoyo.

 

6. NGATI MUFUNA KUDZIWA ZA CHINTHU, PITANI KWA MWINI KUPANGA

 

Mlaliki 6:3

 

CHOLINGA CHOMWE MUKHALIRA NDI MOYO

Ngati munthu sadziwa chifukwa chomwe akhalira padziko amaona imfa ngati chinthu chimodzi chofunikira m’moyo wake. Izi zimachitika kamba koti moyo ngopanda tanthauzo (phindu) kwa iye. Moyo wopanda tanthauzo ndi cholinga ulibe phindu. Kodi moyowu tingaudziwe bwanji? Moyo wopanda tanthauzo ndi moyo wopanda Yesu chifukwa moyo wopanda Yesu ngosowa mtsogoleri. Pa chifukwa ichi , munthu wakhala akuganiza kuti ngoyang’anira moyo wake yekha ganizo lopusa lomwe lapangitsa anthu ambiri kupeza mavuto. Kulakwitsa uku ngakhale kholo lathu Adamu anakuchita poganiza kuti kumvera cholengedwa ndi mbali imodzi yosonyeza kuzindikira. Zotsatira Adamu anagonjera kwa Satana nanyoza malamulo omwe mulungu anawaika pakati pao. Chifukwa cha ichi munthu wakhala akugwiritsa ntchito nthawi yomwe iye anapatsidwa molakwikwa posankha njira ya iye yekha osati yomwe Yesu Khristu wamulangiza, zotsatira zake zake munthu wakhala akuyenda m’moyo wamavuto osaneneka.

 

Nthawi yopanda cholinga imasandulika nthawi yokhumudwa ndi yogwetsedwa mphwayi. Kamba ka ichi nthawi zonse munthu ngogwetsedwa mphwayi pamene azindikira kuti moyo wake wataya nthawi popanda kupindula chirichonse. Anthu ambiri atayika chifukwa chosagwiritsa bwino nthawi yomwe Yehova anawapatsa padziko nakhala okhumudwistidwa m’moyo wao wonse. Tsopano zonsezi zingotizindikiritsa kuti kali konso komwe Mulungu anakalenga kali ndi cholinga ndipo kanaikidwa kuti kakalemekeze Mulungu. Zina mwa zinzindikiro zosonyeza kuti anthu ngogwetsedwa nthawi mvetserani ma wailesi kapena onani pa kanema muona kapena kumva anthu akuzipha, akupha anzao ndi kuchita zinthu zambiri zosonyeza kulowerera. Ndidamvapo anthu ena akufotokoza kuti ziwawa m’dziko kapena kuchuluka kwa uchigawenga ndi mbali imodzi yosonyeza kuti dziko likutukuka, koma ganizo ili liri lopusa komanso lopanda nzeru kamba kakauti chitukuko chikuyenera kubweretsa mtima wakukhutira ndi m’mene zinthu zikupezekera m’dziko kapena pamalo. Kotero munthu atakhala kuti watukuka sangalakelakenso kuba za nzake

akutiza kuti sibwino kudziganizira tokha za m’mene zinthu ziyenera kukhalaira. Tikumva kuti Mulungu analenga zones za padziko la pansi ndi kumwamba ndipo mwini kulengayo anali ndi cholinga malingaliro ake. Mulungu anamulenga munthu n’chifanizo chake nampatsa munthuyo ulamuliro pa zones za padziko ndi mulengalenga nankonzera munthu njira yopuluukirapo ndiye Yesu khristu chifukwa anadziwa kuti munthu adza’chimwira Mulungu.

monga anenera pa Gen.1:1, Mulungu analenga nthawi koma iye sanakhalepo munthawiyo, "Pachiyambi Mulungu analenga" zitanthauza kuti Mulunguyo analipo chiyambicho chisanafike(kusanakhale kuyamba). Izi zitithtandiza kumvetsa kuti Yehova sakhala munthawi ndipo kamba ka ichi Yesu Khristu anati, Iye ali mwini wa dzuwa la sabata. Nthawi inapangidwira munthu osati munthu kupangidwira nthawi n’chifukwa chake ntchito iliyonse ya pamoyo wamunthu njoikikiratu(Job13:1-4). Yohane akutifotokozeranso kuti Genesis kapena kuti Chiyambi ndi zothatira za cholinga.(Yohane1:1) Palibe chomwe chipezeka ndi cholinga chofuna kukongoletsa kapena kupangitsa malo kuoneka bwino koma chiri chonse chiri ncholinga. Mwachitsanso anthu akhala akuganiza kuti maluwa a Rose anapangidwa kuti adzakongoletse dziko, koma akatwiri a science asonyeza kuti duwa la Rose monga chomera chilichonse linaikidwa pa dziko la pansi ndi cholinga. Izo zimapereka mpweya wofunikira kwamunthu kuti azipuma bwino. Taganizani, mpweya womwe uli wofunikira ku moyo wa munthu umachokera ku zomera zomwe ife timaganiza kuti cholinga chake nkukongoletsa basi.


This website was created for free with Own-Free-Website.com. Would you also like to have your own website?
Sign up for free